Child Protection (Chichewa)

Monga membala wa  bungwe la Compassion padziko lonse lapansi, ndinu oyimira ana ndi achinyamata,  ngakhale kuti simugwira ntchito ndi anawo. Pamaphunziro ofunikirawa, muphunzira momwe mungapewele mchitidwe wa nkhanza ndi kuchitapo kanthu pakachitika  nkhanza, kulekeleledwa kapena kugwiritsidwa nthito mosayenera kwa ana ndi achinyamata. Maphunzirowa akuphatikizapo kuvomereza Malamulo akagwilidwe ka ntchito ka Compassion kokhuzana ndi chitetezo cha ana ndi achinyamata. 

Cholinga cha maphunzirowa ndi kupereka mphamvu kwa ophunzira, kutsimikizira kapena kusintha ndondomeko zanu zowunikira anthu ofuna ntchito kuyenera kwawo pogwira ntchito ndi ana. Ifotokoza kufunikira
kwa ndondomeko zolembera anthu ntchito motetezeka ndikuthandiza ophunzira kuwunika kuyenera kwa ofuna ntchito onse pogwira ntchito
ndi othandizidwa.