Mawebusaiti onse a ForChildren.com eniake ndi bungwe la Compassion International ndipo onsewa amafunika kutsatira ndondomeko yokhudza kusunga chinsinsi yopezeka pa www.compassion.com/privacy-policy.htm. Mfundo zachidule zotsatirazi sizikulowa mmalo mwa ndondomeko yathu yaikulu yokhudza kusunga chinsinsi, koma cholinga chake ndi kufotokoza momveka bwino mbali zofunika kuti kudziwe mmene mungagwiritsire ntchito mawebusaiti a ForChildren. Compassion.com imatumikira anthu opereka chithandizo, mabungwe ndi anthu omwe angathe kuyenerera kugwira nafe ntchito, choncho mauthenga otengedwa pa webusaiti ya compassion.com amakhala ochulukirapo poyerekezera ndi a pa ForChildren. ForChildren ndi malo ochitirapo maphunziro, choncho mauthenga omwe amatengedwa kwakukulu amakhala okhudza mmene mumagwiritsira ntchito zinthu zomwe zili pawebusaitiyi. Timasunga mauthengawa kuti akuthandizeni komanso kuthandiza magulu ochita maphunziro kupereka zinthu zogwiritsa ntchito pa maphunziro.
Kodi timatenga mauthenga otani pa ForChildren, nanga n'chifukwa chiyani?
- Ngati mungatsegule akaunti pawebusaiti yathu, timaona zimene mwaona komanso zomwe mwapanga dawunilodi, komanso maphunziro (ma course) omwe mwachita. Timagwiritsa ntchito mauthenga amenewa kuti tikuonetseni mbiri ya zomwe munaona komanso maphunziro omwe mwachitira pamalowa m'mbuyomu. Timagwiritsanso ntchito mauthengawoo kuti tione zinthu zofunikira komanso zinthu zoyenera kuchotsedwa kapena kusinthidwa.
- Ngati muli mbali ya tchalitchi chomwe chinapanga mgwirizano ndi bungwe la Compassion International, maphunziro omwe mungasankhe angathe kuthandiza kuwonjezera chidziwitso chanu pa udindo womwe muli nawo. Webusaitiyi imasunga mauthenga osonyeza kuti inuyo mwachita nawo maphunzirowo. Mauthengawa amathandiza inuyo komanso gulu la opereka maphunziro ku Compassion.
- Pawebusaiti yathu pali ma cookies omwe ndi mauthenga omwe amathandiza kusunga zomwe mwasankha pamalowa. Mwachitsanzo, mawebusaiti athu ena amakupemphani kuti musankhe chinenero chomwe mungakonde komanso amafunika kukumbukira zomwe munasankhazo mukadzalowanso pamalowa. Ma cookies amenewa amasiya kugwira ntchito pakatha maila ochepa choncho funsolo lidzabweranso pa nthawi yomwe mwalowanso pawebusaitiyi, koma osati pa nthawi yomwe mukuona zinthu pamalowa.
- Tilinso ndi ma cookies omwe amasonyeza mwachidule mauthenga okhudza anthu omwe akugwiritsa ntchito malowa komanso zomwe akuchitapo. Malipiti amenewa amagwiritsidwa ntchito pa zolinga zosiyanasiyana, kuphatikizapo kudziwa patsamba omwe ndi otchuka, omwe sakudziwika kwenikweni komanso kudziwa ngati anthu omwe amalowa pawebusaitiyi akugwiritsa ntchito webusaiti yoyenerera kuti azitha kuona mauthenga okhudzana ndi dziko lawo.
Mauthenga omwe a ForChildren amatenga sagulitsidwa ku bungwe lililonse.
Kodi n'zotheka kudilita akaunti ya ForChildren? Inde. Mungathe kudilita nokha patsamba la pulofailo yanu.
Ngati muli ndi mafunso okhudza webusaitiyi, chonde, lankhulani nafe pogwiritsa ntchito fomu ino.
Ngati muli ndi mafunso okhudza ndondomeko yosunga chinsinsi yathuyi, kapena ngati mukufunsa kugwiritsa ntchito ufulu wanu wosunga chinsinsi, chonde lankhulani nafe kudzera pa ndondomeko yaikulu yosunga chinsinsi.